Psalms 100

Salimo. Nyimbo yothokoza.

1Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi.
2Mulambireni Yehova mosangalala;
bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.
3Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.
Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake;
ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.

4Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko
ndi ku mabwalo ake ndi matamando;
muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.
5Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya;
kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.
Copyright information for NyaCCL